15 Kudonthadontha tsiku lamvula,Ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.
16 Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo;Dzanja lace lamanja lingogwira mafuta.
17 Citsulo cinola citsulo;Comweco munthu anola nkhope ya mnzace.
18 Wosunga mkuyu adzadya zipatso zace;Wosamalira ambuyace adzalemekezedwa.
19 Monga m'madzi nkhope zionana,Momwemo mitima ya anthu idziwana.
20 Kunsi kwa manda ndi kucionongeko sikukhuta;Ngakhale maso a munthu sakhutai.
21 Siliva asungunuka m'mbiya,Ndi golidi m'ng'anjo,Motero comwe munthu acitama adziwika naco.