2 Wina akutame, si m'kamwamwako ai;Mlendo, si milomo ya iwe wekha.
3 Mwala ulemera, mcenga ndiwo katundu;Koma mkwiyo wa citsiru upambana kulemera kwace.
4 Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka;Koma ndani angalakike ndi nsanje?
5 Cidzudzulo comveka ciposa cikondi cobisika.
6 Kulasa kwa bwenzi kulikokhulupirika;Koma mdani apsompsona kawiri kawiri.
7 Mtima wokhuta upondereza cisa ca uci;Koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.
8 Monga mbalame yosocera ku cisa cace,Momwemo munthu wosocera ku malo ace.