24 Pakuti cuma siciri cosatha;Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo?
25 Amatuta maudzu, msipu uoneka,Achera masamba a kumapiri,
26 Ana a nkhosa akubveka,Atonde aombolera munda;
27 Mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya;Ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.