8 Monga mbalame yosocera ku cisa cace,Momwemo munthu wosocera ku malo ace.
9 Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima,Ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu,
10 Mnzako, ndi mnzace wa atate wako, usawasiye;Usanke ku nyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako;Mnansi wapafupi aposa mbale wakutari.
11 Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga;Kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.
12 Wocenjera aona zoipa, nabisala;Koma acibwana angopitirira, nalipitsidwa.
13 Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi waciwerewere cikole umgwire mwini.
14 Yemwe adalitsa mnzace ndi mau akuru pouka mamawa,Anthu adzaciyesa cimeneco temberero.