1 Woipaathawapalibewomthamangitsa;Koma olungama alimba mtima ngati mkango.
2 Pocimwa dziko akalonga ace acuruka;Koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikuru.
3 Munthu waumphawi wotsendereza osaukaAkunga mvula yamadzi yokokolola dzinthu.
4 Omwe asiya cilamulo atama oipa;Koma omwe asunga cilamulo akangana nao.
5 Oipa samvetsetsa ciweruzo;Koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.