12 Posekera olungama pali ulemerero wambiri;Koma pouka oipa anthu amabisala.
13 Wobisa macimo ace sadzaona mwai;Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzacitidwa cifundo.
14 Wodala munthu wakuopakosalekeza;Koma woumitsa mtima wace adzagwa m'zoipa.
15 Monga mkango wobangula ndi cirombo coyendayenda,Momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.
16 Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;Koma yemwe ada cisiriro adzatanimphitsa moyo wace.
17 Woparamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;Asamuletse.
18 Woyenda mwangwiro adzapulumuka;Koma wokhota m'mayendedwe ace adzagwa posacedwa.