18 Woyenda mwangwiro adzapulumuka;Koma wokhota m'mayendedwe ace adzagwa posacedwa.
19 Wolima munda wace zakudya zidzamkwanira;Koma wotsata anthu opanda pace umphawi udzamkwanira.
20 Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri;Koma wokangaza kulemera sadzapulumuka cilango,
21 Cetera siliri labwino,Ngakhale kulakwa kuti ukadye kanthu.
22 Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera,Osadziwa kuti umphawi udzamfikira.
23 Adzamkomera mtima wodzudzula m'tsogolo mwace,Koposa wosyasyalika ndi lilime lace.
24 Wobera atate wace, pena amace, nati, Palibe kulakwa;Ndiye mnzace wa munthu wopasula.