5 Oipa samvetsetsa ciweruzo;Koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.
6 Waumphawi woyenda mwangwiroApambana ndi yemwe akhotetsa njira zace, angakhale alemera.
7 Wosunga cilamulo ndiye mwana wozindikira;Koma mnzao wa adyera acititsa atate wace manyazi.
8 Wocurukitsa cuma cace, pokongoletsa ndi phindu,Angokundikira yemwe acitira osauka cisoni.
9 Wopewetsa khutu lace kuti asamve cilamulo,Ngakhale pemphero lace linyansa.
10 Wosoceretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa,Adzagwa mwini m'dzenje lace;Koma angwiro adzalandira colowa cabwino.
11 Wolemera adziyesa wanzeru;Koma wosauka wozindikira aululitsa zace.