1 Mau a Lemueli mfumu, uthenga umene amace anamphunzitsa.
2 Ciani mwananga, Ciani mwana wa mimba yanga?Ciani mwana wa zowinda zanga?
3 Musapereke mphamvu yako kwa akazi,Ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu.
4 Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo;Akalonga sayenera kunena, Cakumwa caukali ciri kuti?
5 Kuti angamwe, naiwale malamulo,Naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.
6 Wofuna kufa umpatse cakumwa caukali,Ndi vinyo kwa owawa mtima;
7 Amwe, narwale umphawi wace, Osakumbukiranso bvuto lace.