1 Mwananga, mvera nzeru yanga;Cherera makutu ku luntha langa;
2 Ukasunge zolingalira,Milomo yako ilabadire zomwe udziwa.
3 Pakuti milomo ya mkazi waciwerewere ikukha uci;M'kamwa mwace muti see koposa mafuta.
4 Cimariziro cace ncowawa ngati civumulo,Ndi cakuthwa ngati lupanga lakuthwa konse konse.
5 Mayendedwe ace atsikira kuimfa;Mapazi ace aumirira kumanda;
6 Sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;Mayendedwe ace adzandira dzandi dzandi osadziwa iye.