14 Ndikadakhala m'zoipa zonse,M'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.
15 Imwa madzi a m'citsime mwako,Ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.
16 Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,Ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?
17 Ikhale ya iwe wekha,Si ya alendo okhala nawe ai.
18 Adalitsike kasupe wako;Ukondwere ndi mkazi wokula nayo.
19 Ngati mbawala yokonda ndi cinkhoma cacisomo,Maere ace akukwanire nthawi zonse;Ukodwe ndi cikondi cace osaleka.
20 Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi waciwerewere,Ndi kufungatira cifuwa ca mkazi wacilendo?