20 Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi waciwerewere,Ndi kufungatira cifuwa ca mkazi wacilendo?
21 Pakuti njira za munthu ziri pamaso pa Yehova,Asinkhasinkha za mayendedwe ace onse.
22 Zoipazacezacezidzagwira woipa;Adzamangidwa ndi zingwe za ucimo wace.
23 Adzafa posowa mwambo;Adzasocera popusa kwambiri.