3 Pakuti milomo ya mkazi waciwerewere ikukha uci;M'kamwa mwace muti see koposa mafuta.
4 Cimariziro cace ncowawa ngati civumulo,Ndi cakuthwa ngati lupanga lakuthwa konse konse.
5 Mayendedwe ace atsikira kuimfa;Mapazi ace aumirira kumanda;
6 Sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;Mayendedwe ace adzandira dzandi dzandi osadziwa iye.
7 Ndipo tsopano ana, mundimvere,Musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga.
8 Siyanitsa njira yako kutari kwa iyeyo,Osayandikira ku khomo la nyumba yace;
9 Kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,Ndi zaka zako kwa ankhanza;