9 Kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,Ndi zaka zako kwa ankhanza;
10 Kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,Ndi kuti usagwire nchito m'nyumba ya wacilendo;
11 Ungalire pa cimariziro cako,Pothera nyama yako ndi thupi lako;
12 Ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,Mtima wanga ndi kunyoza cidzudzulo;
13 Ndipo sindinamvera mau a aphunzitsi anga;Ngakhale kucherera makutu kwa akundilanga mwambo!
14 Ndikadakhala m'zoipa zonse,M'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.
15 Imwa madzi a m'citsime mwako,Ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.