10 Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;
11 Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.
12 Munthu wopanda pace, mwamuna wamphulupulu;Amayenda ndi m'kamwa mokhota;
13 Amatsinzinira ndi maso ace, napalasira ndi mapazi ace,Amalankhula ndi zala zace;
14 Zopotoka ziri m'mtima mwace, amaganizira zoipa osaleka;Amapikisanitsa anthu.
15 Cifukwa cace tsoka lace lidzadza modzidzimuka;Adzasweka msanga msanga, palibe compulumutsa.
16 Ziripo zinthu zisanu ndi cimodzi Mulungu azida;Ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: