16 Ziripo zinthu zisanu ndi cimodzi Mulungu azida;Ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:
17 Maso akunyada, lilime lonama,Ndi manja akupha anthu osacimwa;
18 Mtima woganizira ziwembu zoipa,Mapazi akuthamangira mphulupulu mmangu mmangu;
19 Mboni yonama yonong'ona mabodza,Ndi wopikisanitsa abale.
20 Mwananga, sunga malangizo a atate wako,Usasiye malamulo a mako;
21 Uwamange pamtima pako osaleka;Uwalunze pakhosi pako.
22 Adzakutsogolera ulikuyenda,Ndi kukudikira uli m'tulo,Ndi kulankhula nawe utauka.