2 Wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako,Wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.
3 Cita ici tsono; mwananga, nudzipulumutse;Popeza walowa m'dzanja la mnzako,Pita nudzicepetse, numdandaulire mnzako,
4 Usaone tulo m'maso mwako,Ngakhale kuodzera zikope zako.
5 Dzipulumutse wekha ngati mphoyo ku dzanja la msaki,Ndi mbalame ku dzanja la msodzi.
6 Pita kunyerere, wolesi iwe,Penya njira zao nucenjere;
7 Ziribe mfumu,Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;
8 Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;Nizituta dzinthu zao m'masika.