22 Adzakutsogolera ulikuyenda,Ndi kukudikira uli m'tulo,Ndi kulankhula nawe utauka.
23 Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika;Ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo;
24 Zikucinjiriza kwa mkazi woipa,Ndi ku lilime losyasyalika la mkazi waciwerewere.
25 Asakucititse kaso m'mtima mwako,Asakukole ndi zikope zace.
26 Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamariza ndi nyenyeswa;Ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatari.
27 Kodi mwamuna angatenge moto pa cifuwa cace,Osatentha zobvala zace?
28 Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,Osapsya mapazi ace?