26 Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamariza ndi nyenyeswa;Ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatari.
27 Kodi mwamuna angatenge moto pa cifuwa cace,Osatentha zobvala zace?
28 Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,Osapsya mapazi ace?
29 Comweco wolowa kwa mkazi wa mnzace;Womkhudzayo sadzapulumuka cilango.
30 Anthu sanyoza mbala ikaba,Kuti ikhutitse mtima wace pomva njala;
31 Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;Idzapereka cuma conse ca m'nyumba yace.
32 Wocita cigololo ndi mkazi alibe nzeru;Wofuna kuononga moyo wace wace ndiye amatero.