28 Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,Osapsya mapazi ace?
29 Comweco wolowa kwa mkazi wa mnzace;Womkhudzayo sadzapulumuka cilango.
30 Anthu sanyoza mbala ikaba,Kuti ikhutitse mtima wace pomva njala;
31 Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;Idzapereka cuma conse ca m'nyumba yace.
32 Wocita cigololo ndi mkazi alibe nzeru;Wofuna kuononga moyo wace wace ndiye amatero.
33 Adzalasidwa nanyozedwa;Citonzo cace sicidzafafanizidwa.
34 Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna,Ndipo sadzacitira cifundo tsiku lobwezera cilango.