31 Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;Idzapereka cuma conse ca m'nyumba yace.
32 Wocita cigololo ndi mkazi alibe nzeru;Wofuna kuononga moyo wace wace ndiye amatero.
33 Adzalasidwa nanyozedwa;Citonzo cace sicidzafafanizidwa.
34 Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna,Ndipo sadzacitira cifundo tsiku lobwezera cilango.
35 Sadzalabadira ciombolo ciri conse,Sadzapembedzeka ngakhale ucurukitsa malipo,