5 Dzipulumutse wekha ngati mphoyo ku dzanja la msaki,Ndi mbalame ku dzanja la msodzi.
6 Pita kunyerere, wolesi iwe,Penya njira zao nucenjere;
7 Ziribe mfumu,Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;
8 Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;Nizituta dzinthu zao m'masika.
9 Udzagona mpaka liti, wolesi iwe?Udzauka ku tulo tako liti?
10 Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;
11 Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.