1 Mwananga, sunga mau anga,Ukundike malangizo anga;
2 Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo;Ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.
3 Uwamange pa zala zako,Uwalembe pamtima pako;
4 Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongwanga;Nuche luntha mbale wako.
5 Kuti zikucinjirizire kwa mkazi waciwerewere,Kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ace.