13 Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona;Nati kwa iye ndi nkhope yacipongwe,
14 Nsembe za mtendere ziri nane;Lero ndacita zowinda zanga.
15 Cifukwa cace ndaturuka kudzakucingamira,Kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.
16 Ndayala zopfunda pakama panga,Nsaru zamangamanga za thonje la ku Aigupto,
17 Ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhiraA mvunja ndi cisiyo ndi mtanthanyerere.
18 Tiye tikondwere ndi cikondano mpaka mamawa;Tidzisangalatse ndi ciyanjano.
19 Pakuti mwamuna kulibe kwathu,Wapita ulendo wa kutari;