16 Ndayala zopfunda pakama panga,Nsaru zamangamanga za thonje la ku Aigupto,
17 Ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhiraA mvunja ndi cisiyo ndi mtanthanyerere.
18 Tiye tikondwere ndi cikondano mpaka mamawa;Tidzisangalatse ndi ciyanjano.
19 Pakuti mwamuna kulibe kwathu,Wapita ulendo wa kutari;
20 Watenga thumba la ndalama m'dzanja lace,Tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.
21 Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace,Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace.
22 Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa;Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru;