19 Pakuti mwamuna kulibe kwathu,Wapita ulendo wa kutari;
20 Watenga thumba la ndalama m'dzanja lace,Tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.
21 Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace,Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace.
22 Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa;Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru;
23 Mpaka mubvi ukapyoza mphafa yace;Amtsata monga mbalame yotamangira msampha;Osadziwa kuti adzaononga moyo wace.
24 Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,Labadirani mau a m'kamwa mwanga.
25 Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo,Usasocere m'mayendedwe ace.