21 Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace,Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace.
22 Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa;Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru;
23 Mpaka mubvi ukapyoza mphafa yace;Amtsata monga mbalame yotamangira msampha;Osadziwa kuti adzaononga moyo wace.
24 Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,Labadirani mau a m'kamwa mwanga.
25 Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo,Usasocere m'mayendedwe ace.
26 Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa;Ndipo ophedwa ndi iye acurukadi.
27 Nyumba yace ndiyo njira ya kumanda,Yotsikira ku zipinda za imfa.