4 Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongwanga;Nuche luntha mbale wako.
5 Kuti zikucinjirizire kwa mkazi waciwerewere,Kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ace.
6 Pakuti pa zenera la nyumba yangaNdinapenyera pa made ace;Ndinaona pakati pa acibwana,
7 Ndinazindikira pakati pa ang'onoMnyamata wopanda nzeru,
8 Alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo,Ndi kuyenda pa njira ya ku nyumba yace;
9 Pa madzulo kuli sisiro,Pakati pa usiku pali mdima,
10 Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira,Atabvala zadama wocenjera mtima,