7 Ndinazindikira pakati pa ang'onoMnyamata wopanda nzeru,
8 Alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo,Ndi kuyenda pa njira ya ku nyumba yace;
9 Pa madzulo kuli sisiro,Pakati pa usiku pali mdima,
10 Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira,Atabvala zadama wocenjera mtima,
11 Ali wolongolola ndi wosaweruzika,Mapazi ace samakhala m'nyumba mwace.
12 Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo,Nabisalira pa mphambano zonse.
13 Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona;Nati kwa iye ndi nkhope yacipongwe,