9 Onsewo amveka ndi iye amene azindikira;Alungama kwa akupeza nzeru.
10 Landirani mwambo wanga, si siliva ai;Ndi nzeru kopambana ndi golidi wosankhika.
11 Pakuti nzeru iposa ngale,Ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo,
12 Ine Nzeru ndikhala m'kucenjera, ngati m'nyumba yanga;Ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.
13 Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa;Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
14 Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa;Ndine luntha; ndiri ndi mphamvu.
15 Mwa ine mafumu alamulira;Akazembe naweruza molungama.