4 Wacibwana yense apambukire kuno;Iti kwa yense wosowa nzeru,
5 Tiyeni, idyani cakudya canga;Nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza.
6 Lekani, acibwana inu, nimukhale ndi moyo;Nimuyende m'njira ya nzeru.
7 Woweruza munthu wonyoza adzicititsa yekha manyazi;Yemwe adzudzula wocimwa angodetsa mbiri yace yace.
8 Usadzudzule wonyoza kuti angakude;Dzudzula wanzeru adzakukonda.
9 Ukacenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yace;Ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira,
10 Ciyambi ca nzeru ndico kuopa Yehova;Kudziwa Woyerayo ndiko luntha;