8 Usadzudzule wonyoza kuti angakude;Dzudzula wanzeru adzakukonda.
9 Ukacenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yace;Ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira,
10 Ciyambi ca nzeru ndico kuopa Yehova;Kudziwa Woyerayo ndiko luntha;
11 Pakuti mwa ine masiku ako adzacuruka,Zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.
12 Ukakhala wanzeru, si yako yako nzeruyo?Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.
13 Utsiru umalongolola,Ngwa cibwana osadziwa kanthu.
14 Ukhala pa khomo la nyumba yace,Pampando pa misanje ya m'mudzi