28 Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; cita ici, ndipo udzakhala ndi moyo.
29 Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?
30 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a acifwamba amene anambvula zobvala, namkwapula, nacoka atamsiya wofuna kufa.
31 Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali yina.
32 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali yina.
33 Koma Msamariya wina ali pa ulendo wace anadzapali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa cifundo,
34 nadza kwa iye, namanga mabala ace, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yace ya iye yekha, nadza naye ku nyumba ya alendo, namsungira.