Luka 4 BL92

Kuyesedwa kwa Yesu

1 Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.

2 Ndipo iye sanadya kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

3 Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.

4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.

5 Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono.

6 Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: cifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.

7 Cifukwa cace ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

8 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,Ndipo iye yekha yekha uzimtumikira,

9 Ndipo anamtsogolera iye ku Yerusalemu, namuika iye pamwamba pa cimbudzi ca Kacisiyo, nati kwa iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;

10 pakuti kwalembedwa, kuti,Adzalamulira angelo ace za, iwe, kuti akucinjirize,

11 Ndipo,Pa manja ao adzakunyamula iwe,Kuti ungagunde konse phazi lako pamwala,

12 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,Usamuyese Ambuye Mulungu wako,

13 Ndipo mdierekezi, m'mene adamariza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi yina.

Yesu aphunzitsa ku Nazarete nacotsedwako

14 Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yace ya iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

15 Ndipo iye anaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.

16 Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.

17 Ndipo anapereka kwa iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,

18 Mzimu wa Ambuye uli paine,Cifukwa cace iye anandidzozaIne ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe,Ndi akhungu kuti apenyenso,Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,

19 Kulalikira caka cosankhika ca Ambuye.

20 Ndipo m'mene iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa iye.

21 Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.

22 Ndipo onse anamcitira iye umboni nazizwa ndi mau a cisomo akuturuka m'kamwa mwace; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

23 Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadziciritsa wekha: zonse zija tazimva zinacitidwa ku Kapernao, muzicitenso zomwezo kwanu kuno.

24 Ndipo iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika ku dziko la kwao.

25 Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'lsrayeli masiku ace a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikuru pa dziko lonselo;

26 ndipo Eliya sanatumidwa kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoniya, kwa mkazi wamasiye.

27 Ndipo munali akhate ambiri m'Israyeli masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Namani yekha wa ku Suriya.

28 Ndipo onse a m'sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi;

29 nanyamuka na mturutsira Iye kunja kwa mudziwo, nanka naye pamutu pa phiri pamene panamangidwa mudzi wao, kuti akamponye iye pansi.

30 Koma iye anapyola pakati pao, nacokapo.

Yesu aciritsa munthu wogwidwa ndi mzimu woipa

31 Ndipo iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya, Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi ciphunzitso cace;

32 cifukwa mau ace anali ndi ulamuliro.

33 Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala naco ciwanda conyansa; napfuula ndi mau olimba, kuti,

34 Ha! tiri ndi ciani ndi Inu, Yesu wa ku N azarete? kodi munadza kutiononga ife? ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wace wa Mulungu.

35 Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nuturuke mwa iye. Ndipo ciwandaco m'mene cinamgwetsa iye pakati, cinaturuka mwa iye cosampweteka konse.

36 Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzace, nanena, Mau amenewa ali otani? cifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingoturuka.

37 Ndipo mbiri yace ya iye inafalikira ku malo onse a dziko Ioyandikira.

Yesu aciritsa mpongozi wa Simoni

38 Ndipo iye ananyamuka kucokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wace wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.

39 Ndipo iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.

40 Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundu mitundu, anadza nao kwa iye; ndipo iye anaika manja ace pa munthu ali yense wa iwo, nawaciritsa.

41 Ndi ziwanda zomwe zinaturuka mwa ambiri, ndi kupfuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, cifukwa zinamdziwa kuti iye ndiye Kristu.

42 Ndipo kutaca anaturuka iye nanka ku malo acipululu; ndi makamu a anthu analikwnfunafuna iye, nadza nafika kwa iye, nayesa kumletsa iye, kuti asawacokere.

43 Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi yinanso: cifukwa ndinatumidwa kudzatero.

44 Ndipo iye analikulalikira m'masunagoge a ku Galileya.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24