Luka 1 BL92

1 POPEZA ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinacitika pakati pa ife,

2 monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,

3 kuyambira paciyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira paciyambi, kulembera kwa iwe tsatane tsatane, Teofilo wabwinotu iwe;

4 kuti udziwitse zoona zace za mau amene unaphunzira.

Aneneratu za kubadwa kwa Yohane

5 Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wace wa ana akazi a pfuko la Aroni, dzina lace Elisabeti.

6 Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa.

7 Ndipo analibe mwana, popeza Elisabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.

8 Ndipo panali, pakucita iye nchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lace, pamaso pa Mulungu, monga mwa macitidwe a kupereka nsembe,

9 adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kacisi wa Ambuye.

10 Ndipo khamu lonse la anthu Iinalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.

11 Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira ku dzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.

12 Ndipo Zakariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.

13 Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane.

14 Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwace.

15 Pakuti iye adzakhala wamkuru pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena, kacasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.

16 Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.

17 Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.

18 Ndipo Zakariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ici ndi ciani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zace za mkazi wanga zacuruka.

19 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, ine ndine Gabrieli, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.

20 Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzacitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau, anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yace.

21 Ndipo anthu analikulindira Zakariya, nazizwa ndi kucedwa kwace m'kacisimo.

22 Koma m'mene iye anaturukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kacisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.

23 Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wace anamarizidwa, anamuka kunyumba kwace.

24 Ndipo atatha masiku awa, Elisabeti mkazi wace anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,

25 Ambuye wandicitira cotero m'masiku omwe iye anandipenyera, kucotsa manyazi anga pakati pa anthu.

Aneneratu za kubadwa kwa Yesu

26 Ndipo mwezi wacisanu ndi cimodzi mngelo Gabrieli anatumidwa ndi Mulungu kunka ku mudzi wa ku Galileya dzina lace N azarete,

27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lace Yosefe, wa pfuko la Davine; ndipo dzina lace la namwaliyo ndilo Mariya.

28 Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wocitidwa cisomo, Ambuye ali ndi iwe.

29 Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulankhula uku nkutani.

30 Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Mariya; pakuti wapeza cisomo ndi Mulungu.

31 Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamucha dzina lace Yesu.

32 Iye adzakhala wamkuru, nadzachedwa Mwana wa Wamkurukuru: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wacifumu wa Davine atate wace:

33 ndipo iye adzacita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wace sudzatha.

34 Koma Mariya anati kwa mngelo, ici cidzacitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?

35 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.

36 Ndipo taona, Elisabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wace; ndipo mwezi uno uli wacisanu ndi cimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

37 Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

38 Ndipo Mariya anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anacoka kwa iye.

Mariya aceza kwa Elisabeti

39 Ndipo Mariya ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi cangu ku dziko la mapiri ku mudzi wa Yuda;

40 nalowa m'nyumba ya Zakariya, nalankhula Elisabeti.

41 Ndipo panali pamene Elisabeti anamva kulankhula kwace kwa Mariya, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwace; ndipo Elisabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;

42 nakweza mau ndi mpfuu waukuru, nati, 2 Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo codalitsika cipatso ca mimba yako,

43 Ndipo ici cicokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amace wa Ambuye wanga?

44 Pakuti ona, pamene mau a kulankhula kwako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.

45 Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; cifukwa zidzacitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.

Nyimbo ya Mariya

46 3 Ndipo Mariya anati,Moyo wanga ulemekeza Ambuye,

47 Ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

48 Cifukwa iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wace;Pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzandichula ine wodala.

49 Cifukwa iye Wamphamvuyo anandicitira ine zazikuru;4 Ndipo dzina lace liri loyera.

50 5 Ndipo cifundo cace cifikira anthu a mibadwo mibadwoPa iwo amene amuopa iye.

51 Iye anacita zamphamvu ndi mkono wace;6 Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao,

52 iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yacifumu,Ndipo anakweza aumphawi,

53 7 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino,Ndipo eni cuma anawacotsa opanda kanthu.

54 Anathangatira Israyeli mnyamata wace,Kuti akakumbukile cifundo,

55 8 (Monga analankhula kwa makolo athu)Kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace ku nthawi yonse.

56 Ndipo Mariya anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwace.

Kubadwa kwa Yohane Mbatizi

57 Ndipo inakwanira nthawi ya Elisabeti, ya kubala kwace, ndipo anabala mwana wamwamuna.

58 Ndipo anansi ace ndi abale ace anamva kuti Ambuye anakulitsa cifundo cace pa iye; 9 nakondwera naye pamodzi.

59 Ndipo panali 10 tsiku lacisanu ndi citatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amuche dzina la atate wace Zakariya.

60 Ndipo amace anayankha, kuti, lai; koma 11 adzachedwa Yohane.

61 Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene achedwa dzina ili.

62 Ndipo anakodola atate wace, afuna amuche dzina liti?

63 Ndipo iye anafunsa colemberapo, nalemba, kuti, Dzina lace ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse.

64 Ndipo 12 pomwepo panatseguka pakamwa pace, ndi lilume lace linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.

65 Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko: lonse la mapiri a Yudeya,

66 Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nangamwana uyu adzakhala wotani? Pakuti 13 dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.

Nyimbo ya Zakariya

67 Ndipo atate wace Zakariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,

68 Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israyeli;14 Cifukwa iye anayang'ana, nacitira anthu ace ciombolo,

69 Ndipo iye anatikwezera ife nyanga ya cipulumutso,Mwa pfuko la Davine mwana wace,

70 15 (Monga iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ace oyera mtima, a kale lomwe),

71 Cipulumutso ca adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife;

72 16 Kucitira atate athu cifundo, Ndi kukumbukila pangano lace lopatulika;

73 Cilumbiro cimene iye anacilumbira kwa Abrahamu atate wathu,

74 Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu,17 Tidzamtumikira iye, opanda mantha,

75 18 M'ciyero ndi cilungamo pamaso pace, masiku athu onse.

76 19 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu:20 Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace;

77 Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso,21 Ndi makhululukidwe a macimoao,

78 Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;

79 22 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa;Kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

80 Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wace, ndipo 23 iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24