Luka 19 BL92

Zakeyu asandulika mtima

1 Ndipo analowa, napyola pa Yeriko. Ndipo taonani, mwamuna wochedwa dzina lace Zakeyu;

2 ndipo Iye anali mkulu wa amisonkho, nali wacuma.

3 Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sana the, cifukwa ca khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu.

4 Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona iye; pakuti anati apite njira yomweyi.

5 Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.

6 Ndipo anafulumira, natsika, namlandira iye wokondwera.

7 Ndipo m'mene anaciona anadandaula onse, nanena, Analowa amcereze munthu ali wocimwa.

8 Ndipo Zakeyu anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.

9 Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero cipulumutso cagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.

10 Pakuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa, cotayikaco.

Fanizo la ndarama khumi

11 Ndipo pakumva izi iwo, iye anaonjeza nanena fanizo, cifukwa anali iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.

12 Pamenepo: anati, Munthu wa pfuko lomveka ananka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.

13 Ndipo anaitana akapolo ace khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Cita nazoni malonda kufikira ndibweranso.

14 Koma mfulu za pamudzi pace zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyu akhale mfumu yathu.

15 Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pocita malonda.

16 Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu inacita nionjeza ndalama khumi.

17 Ndipo anati kwa iye, Cabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'cacing'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.

18 Ndipo anadza waciwiri, nanena, Mbuye, ndalama yanu yapindula ndalama zisanu.

19 Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu.

20 Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi ndalama yanu, ndaisunga m'kansaru;

21 pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula cimene simunaciika pansi, mututa cimene simunacifesa.

22 Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula cimene sindinaciika, ndi wotuta cimene sindinacifesa;

23 ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lace?

24 Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mcotsereni ndalamayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo ndalama khumi.

25 Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo ndalama khumi.

26 Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala naco kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, cingakhale cimene ali naco cidzacotsedwa.

27 Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani cao kuno, nimuwaphe pamaso panga,

28 Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.

Yesu alowa m'Yerusalemu

29 Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lochedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,

30 nati, Mukani ku mudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa buru womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iri yonse; mummasule iye nimumtenge.

31 Ndipomunthuakati kwa inu, Mummasuliranji? mudzatero naye, Ambuye amfuna iye.

32 Ndipo anacoka otumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo.

33 Ndipo pamene anamasula mwana wa buru, eni ace anati kwa iwo, Mumasuliranji mwana wa buru?

34 Ndipo anati, Ambuye amfuna iye.

35 Ndipo anadzanave kwa Yesu; ndipo anayalika zobvala zao pa mwana wa buruyo, nakwezapo Yesu.

36 Ndipo pakupita iye, anayala zobvala zao m'njira.

37 Ndipo pakuyandikira iye tsono potsetsereka pace pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akuru, cifukwa ca nchito zonse zamphamvu anaziona;

38 nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere m'Mwamba, ndi ulemerero m'Mwambamwamba.

39 Ndipo Afarisi ena a m'khamu la anthu anati kwa iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.

40 Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa akhala cete miyala idzapfuula.

Yesu alirira Yerusalemu

41 Ndipo m'meneanayandikira, anaona mudziwo naulirira,

42 nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! koma tsopano zibisika pamaso pako.

43 Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;

44 ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzace; popeza sunazindikira nyengo, ya mayang'aniridwe ako.

Ayeretsa kacisi kaciwiri

45 Ndipo analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao,

46 Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa iyo phanga la acifwamba.

47 Ndipo analikuphunzitsa m'Kacisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga iye;

48 ndipo sanapeza cimene akacita; pakuti anthu onse anamlendewera iye kuti amve.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24