Luka 15 BL92

Fanizo la nkhosa yosokera

1 Koma amisonkho onse ndi anthu ocimwa analikumyandikira kudzamva iye.

2 Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ocimwa, nadya nao.

3 Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena,

4 Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'cipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?

5 Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ace wokondwera.

6 Ndipo pakufika kunyumba kwace amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena nao, Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.

7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Fanizo la ndarama yotayika

8 Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yace, nafunafuna cisamalire kufikira akaipeza?

9 Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena; Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.

10 Comweco, ndinena kwa inu, kuli cimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu cifukwa ca munthu wocimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

Fanizo la mwana wolowerera

11 Ndipo iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri;

12 ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wace, Atate, ndigawirenitu zanga za pa cuma canu. Ndipo iye anawagawira za moyo wace.

13 Ndipo pakupita masiku owerengekamwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wace ku dziko lakutari; ndipo komweko anamwaza cuma cace ndi makhalidwe a citayiko.

14 Ndipo pamene anatha zace zonse, panakhala njala yaikuru m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.

15 Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwace kukaweta nkhumba.

16 Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yace ndi makoko amene nkhumba rimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.

17 Koma m'mene anakumbukila mumtima, anati, Anchito olipidwa ambiri a atate wanga ali naco cakudya cocuruka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

18 Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena nave, Atate, ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu;

19 sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa anchito anu.

20 Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wace. Koma pakudza iye kutali, atate wace anamuona, nagwidwa cifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pace, nampsompsonetsa.

21 Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu.

22 Koma atateyo ananena kwaakapolo ace, Turutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni phete ku dzanja lace ndi nsapato ku apazi ace;

23 ndipo idzani naye mwana wa ng'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;

24 cifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.

25 Koma mwana wace wamkuru anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuyimba ndi kubvina.

26 Ndipo anaitana mmodzi wa anayamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?

27 Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwana wa ng'ombe wonenepa, cifukwa anamlandira iye wamoyo.

28 Koma anakwiya, ndipo sanafuna kulowamo, Ndipo atate wace anaturuka namdandaulira.

29 Koma anayankha nati kwa atate wace, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthawi iri yonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.

30 Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi aciwerewere, munamphera iye mwana wa ng'ombe wonenepa.

31 Koma iye ananena nave, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako.

32 Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: cifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24