Luka 18 BL92

Fanizo la woweruza wosalungama

1 Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima;

2 nanena, M'mudzi mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu.

3 Ndipo m'mudzimo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane.

4 Ndipo sanafuna nthawi; koma bwino bwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu;

5 koma cifukwa ca kundibvuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwace.

6 Ndipo Ambuye anati, Tamverani conena woweruza wosalungama.

7 Ndipo kodi Mulungu sadzacitira cilungamo osankhidwa ace akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?

8 Ndinena ndi inu, adzawacitira cilungamo posacedwa. Koma Mwana wa munthu pakudza Iye, vadzapeza cikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?

Fanizo la Mfarisi ndi wamsonkho

9 Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,

10 Anthu awiri anakwera kunka kukacisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzace wamsonkho.

11 Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, acigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;

12 ndisala cakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi lamagawo khumi la zonse ndiri nazo.

13 Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pacifuwa pace nanena, Mulungu, mundicitire cifundo, ine wocimwa.

14 Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwace woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzacepetsedwa; koma wodzicepetsa yekha adzakulitsidwa.

Yesu adalitsa ana

15 Ndipo anadzanao kwa iye ana amakanda kuti awakbudze; koma pamene ophunzira anaona, anawadzudzula.

16 Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uti wa otere.

17 Indetu ndinena kwa inu, Ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

Mkuru mwini cuma

18 Ndipo mkuru wina anamfunsa iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizicita ciani, kuti ndilowe moyo wosatha?

19 Koma Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.

20 Udziwa malamulo. Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usacite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.

21 Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga.

22 Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa cinthu cimodzi: gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala naco cuma ceni ceni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

23 Koma pakumva izi anagwidwa naco cisoni cambiri; pakuti anali mwini cuma cambiri.

24 Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! nkubvutika nanga kwa anthu eni cuma kulowa Ufumu wa Mulungu!

25 Pakuti nkwapafupi kwa ngamila apyole diso la singano koma kwa munthu mwini cuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.

26 Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa?

27 Koma iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

28 Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu.

29 Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akumbala, kapena ana, cifukwa ca Ufumu wa Mulungu,

30 koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi yino; ndipo m'nthawi irinkudza moyo wosatha.

Yesu aneneratu za mazunzo ace

31 Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunkaku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.

32 Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamcitira cipongwe, nadzamthira malobvu; ndipo atamkwapula adzamupha iye;

33 ndipo tsiku lacitatu adzauka.

34 Ndipo sanadziwitsa kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikira zonenedwazo.

Msaona wa ku Yeriko

35 Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha;

36 ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, ici nciani?

37 Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.

38 Ndipo anapfuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.

39 Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale cete; koma iye anapfuulitsa cipfuulire, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.

40 Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa iye: ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye,

41 Of una ndikucitire ciani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso.

42 Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.

43 Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anacitira Mulungu mayamiko.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24