Luka 12 BL92

Yesu awacenjeza za cinyengo

1 Pomwepo pamene anthu a zikwi zikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, iye anayamba kunena kwa ophunzira ace poyamba, Tacenierani nokha ndi cotupitsa mikate ca Afarisi, cimeneciri cinyengo.

2 Koma kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

3 Cifukwa cace zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo cimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati cidzalalikidwa pa macindwi a nyumba.

A wachulira amene ayenera kumuopa

4 Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ici alibe kanthu kena angathe kucita.

5 Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kugehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.

6 Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;

7 komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wace wa mpheta zambiri.

8 Ndipo ndinena kwa inu, Amene ali yense akabvomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa munthu adzambvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu;

9 koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.

10 Ndipo amene ali yense adzanenera Mwana wa munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

11 Ndipo pamene pali ponse adzamuka nanu ku mlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena ciani;

12 pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

Fanizo La mwini cuma wopusa

13 Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine cuma camasiye.

14 Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?

15 Ndipo iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uli wonse; cifukwa moyo wace wa munthu sulingana ndi kucuruka kwa zinthu zace ali nazo.

16 Ndipo iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wace wa munthu mwini cuma unapatsa bwino.

17 Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga?

18 Ndipo anati, Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikuru, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi cuma canga.

19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli naco cuma cambiri cosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

20 Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?

21 Atero iye wakudziunjikira cuma mwini yekha wosakhala naco cuma ca kwa Mulungu,

Nkhawa za mayo wathu

22 Ndipo Iyeanati kwa ophunzira ace, Cifukwa cace ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, cimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, cimene mudzabvala.

23 Pakuti moyo uli woposa cakudya, ndi thupi liposa cobvala.

24 Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa: nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

25 Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wace?

26 Kotero ngati simungathe ngakhale cacing'onong'ono, muderanji nkhawa cifukwa ca zina zija?

27 Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa nchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wace wonse, sanabvala ngati limodzi la awa.

28 Koma ngati Mulungu abveka kotere maudzu a kuthengo akukhala lero, ndipo mawa aponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?

29 Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31 Komatu tafuna-funani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.

32 Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34 Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Fanizo La kapolo wocezera

35 Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36 ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37 Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38 Ndipo akadza ulonda waciwiri, kapena wacitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39 Koma zindikirani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yace yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yace ibooledwe.

40 Khalani okonzeka inunso; cifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.

41 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

42 Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace adzamuika kapitao wa pa banja lace, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yace?

43 Wodala kapoloyo amene mbuye wace pakufika, adzampeza alikucita cotero.

44 1 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.

45 Koma 2 kapolo uyo akanena mumtima mwace, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;

46 3 mbuye wa kapolouyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati, nadzamuika dera lace pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

47 Ndipo 4 kapolo uyo, wodziwa cifuniro ca mbuye wace, ndipo sanakonza, ndi kusacita zonga za cifuniro caceco, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.

48 Koma 5 iye amene sanacidziwa, ndipo anazicita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu ali yense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.

Yesu aponya moto pa dsiko lapansi

49 Ine ndinadzera kuponya mota pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji, ngati unatha kuyatsidwa?

50 Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

51 Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapani? Ndinena wa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;

52 pakuti 6 kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

53 Adzatsutsana atate ndi mwana wace, ndi mwana ndi atate wace; amace adzatsutsana ndi mwana wamkazi'l ndi mwana wamkazi ndi amace, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wace, ndi mkaziyo ndi mpongozi wace.

Zizindikilo za nyengo yace

54 Koma iye ananenanso kwa makamu a anthu, 7 Pamene pali ponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero.

55 Ndipo pamene mphepo ya kumwela iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yace ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengoyino?

57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

58 Pakuti 8 pamene ulikupita naye mnzako wa miandu kwa woweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, ndi msilikari angaponye iwe m'nyumba yandende.

59 Ine ndinena kwa iwe, 9 Sudzaturukamo konse kufikira utalipira kakobiri kakumariza.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24