Luka 16 BL92

Fanizo la kapitao wonyenga

1 Ndipo iye ananenanso kwa ophunzira ace, Panali munthu mwini cuma, anali ndi kapitao wace; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza cuma cace.

2 Ndipo anamuitana, nati kwa iye, ici ndi ciani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.

3 Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwace, Ndidzacita ciani, cifukwa mbuye wanga andicotsera ukapitao? kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundicititsa manyazi.

4 Ndidziwa cimene ndidzacita, kotero kuti pamene ananditurutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao.

5 Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wace, nanena kwa woyamba, Unakongola ciani kwa mbuye wanga?

6 Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.

7 Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Mitanga ya tirigu zana iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu.

8 Ndipo mbuye wace anatama kapitao wonyengayo, kuti anacita mwanzeru; cifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.

9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi cuma cosalungama; kuti pamene cikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.

10 Iye amene akhulupirika m'cacing'onong'ono alinso wokhulupirika m'cacikuru; ndipo iye amene ali wosalungama m'cacing'onong'ono alinso wosalungama m'cacikuru.

11 Cifukwa cace ngati simunakhala okhulupirika m'cuma ca cosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi cuma coona?

12 Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zace za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

13 Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.

Za mphamvu ya cilamulo

14 Koma Marisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.

15 Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; cifukwa ici cimene cikuzika mwa anthu ciri conyansa pamaso pa Mulungu.

16 Cilamulo ndi aneneci analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu ali yense akangamira kulowamo.

17 Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zicoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono ka cilamulo kagwe nkwapatali.

18 Yense wakusudzula mkazi wace, nakwatira wina, acita cigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, acita cigololo,

Fanizo la mwini cuma ndi Lazaro waumphawi

19 Ndipo panali munthu mwini cuma amabvala cibakuwa ndi nsaru yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;

20 ndipo wopemphapempha wina, dzina lace Lazaro, adaikidwa pakhomo pace wodzala ndi zironda,

21 ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini cumayo; komatu agarunso anadza nanyambita zirondazace.

22 Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka ku cifuwa ca Abrahamu; ndipo mwini cumayo adafanso, naikidwa m'manda.

23 Ndipo m'Hade anakweza maso ace, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'cifuwa mwace.

24 Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundicitire cifundo, mutome Lazaro, kuti abviike nsonga ya cala cace m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.

25 Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukila kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.

26 Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikuru, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kucokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kucokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.

27 Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume ku nyumba ya atate wanga;

28 pakuti ndirinao abale asanu; awacitire umboni iwo kuti iwonso angadze ku malo ana a mazunzo.

29 Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.

30 Koma anati, lai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wocokera kwa akufa adzasandulika mtima.

31 Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24