Luka 10 BL92

Yesu atuma ophunzira makumi asanu ndi awiri

1 Zitatha izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiri awiri pamaso pace ku mudzi uli wonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

2 Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzicuruka, koma anchito acepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe anchito kukututa kwace.

3 Mukani; taonani, Ine ndituma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu.

4 Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalankhule munthu panjira.

5 Ndipo m'nyumba iri yonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.

6 Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.

7 Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wanchito ayenera mphotho yace; musacokacoka m'nyumba.

8 Ndipo m'mudzi uli wonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;

9 ndipo ciritsani odwala ali mamwemonimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma ku mudzi uli wonse mukalowako,

10 ndipo salandira inu, m'mene mwaturuka ku makwalala ace nenani,

11 Lingakhale pfumbi locokera kumudzi kwanu, lomamatika ku mapaziathu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ici, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.

12 Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodoma kudzapiririka kuposa mudzi umenewo.

13 Tsoka iwe, Korazini! tsoka iwe Betsaida! cifukwa kuti zikadacitika m'Turo ndi Sidoni zamphamvuzi zidacitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi obvala ciguduli ndi phulusa.

14 Koma ku Turo ndi Sidoni kudzapiririka m'ciweruziro, koposa inu.

15 Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku Hade,

16 iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana iye amene anandituma Ine.

17 Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.

18 Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wocokera kumwamba.

19 Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iri yonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

20 Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba.

21 Nthawi yomweyo iye anakondwera ndi Mzimu Wovera, nati, Ndikubvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

22 Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira iye.

23 Ndipo m'mene anapotolokera kwa ophunzira ace, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona.

24 Pakuti ndinena ndi inu kuti 1 aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu muziona, koma sanaziona; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimva.

Fanizo La Msamariya wacifundo

25 Ndipo taonani, wacilamulo wina anaimirira namuyesa iye, nanena, 2 Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kucita ciani?

26 Ndipo anati kwa iye, M'cilamulo mulembedwa ciani? Uwerenga bwanji?

27 Ndipo iye anayankha nati, 3 Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.

28 Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; cita ici, ndipo udzakhala ndi moyo.

29 Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?

30 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a acifwamba amene anambvula zobvala, namkwapula, nacoka atamsiya wofuna kufa.

31 Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali yina.

32 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali yina.

33 Koma Msamariya wina ali pa ulendo wace anadzapali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa cifundo,

34 nadza kwa iye, namanga mabala ace, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yace ya iye yekha, nadza naye ku nyumba ya alendo, namsungira.

35 Ndipo m'mawa mwace anaturutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo ciri conse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.

36 Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a acifwamba?

37 Ndipo anati, iye wakumcitira cifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita, nucite iwe momwemo.

Marita ndi Mariya

38 Ndipo pakupita paulendo pao iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lace 4 Marita anamlandira iye kunyumba kwace.

39 Ndipo anali ndi mbale wace wochedwa Mariya, ndiye wakukhala pa mapazi a Ambuye, namva mau ace.

40 Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.

41 Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nubvutika ndi zinthu zambiri;

42 koma cisoweka cinthu cimodzi, pakuti Mariya anasankha dera lokoma limene lsilidzacotsedwa kwa iye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24