Luka 23 BL92

Yesu na bwalo la Pilato

1 Ndipo khamu lonselo Iinanyamuka kupita naye kwa Pilato.

2 Ndipo anayamba kumnenera iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Kristu mfumu.

3 Ndipo Pilato anamfunsa iye, nanena, Kodindiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo iye anamyankha nati, Mwatero.

4 Ndipo Pilato anati kwa ansembe akuru ndi makamu a anthu, Ndiribe kupeza cifukwa ca mlandu ndi munthu uyu.

5 Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa m'Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.

6 Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya.

7 Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa m'ulamuliro wace wa Herode, anamtumiza iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa,

Yesu atumidwa kwa Herode

8 Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya iye, cifukwa anamva za iye; nayembekeza kuona cizindikilo cina cocitidwa ndi iye.

9 Ndipo anamfunsa iye mau ambiri; koma iye sanamyankha kanthu.

10 Ndipo ansembe akuru ndi alembi anaimirira, namnenera iye kolimba.

11 Ndipo Herode ndi asilikari ace anampeputsa iye, namnyoza, nambveka iye copfunda conyezimira, nambwezera kwa Pilato.

12 Ndipo Herode ndi Pilato anaci-I tana cibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana.

Yesu abwezedwa kwa Pilato. Baraba amasulidwa. Yesu amangidwa

13 Ndipo Pilato anaitana ansembe akuru, ndi akuru, ndi anthu, asonkhane,

14 nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu cifukwa ca zinthu zimene mumnenera;

15 inde, nga khale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera iye kwa ife; ndipo taonani, sanacita iye kanthu kakuyenera kufa.

16 Cifukwacace ndidzamkwapula ndi kununasula iye. [

17 ]

18 Koma iwo onse pamodzi anapfuula, nati, Cotsani munthu uyu, mutimasulire Baraba;

19 ndiye munthu anaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko m'mudzi ndi ca kupha munthu.

20 Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;

21 koma iwo anapfuula, nanena, Mpacikeni, mpacikeni pamtanda.

22 Ndipo anati kwa iwo nthawi yacitatu, Nanga munthuyu anacita coipa ciani? Sindinapeza cifukwa ca kufera iye; cotero ndidzamkwapula iye ndi kummasula.

23 Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti iye apacikidwe, Ndipo mau ao analakika.

24 Ndipo Pilato anaweruza kuti cimene alikufunsa cicitidwe.

25 Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa cifuniro cao.

Yesu pa njira ya ku Golgota

26 Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pace pa Yesu,

27 Ndipo unamtsata unyinji waukuru wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pacifuwa, namlirira iye.

28 Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.

29 Cifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.

30 Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.

31 Pakuti ngati azicitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?

32 Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ocita zoipa; anatengedwa pamodzi ndi iye kuti aphedwe.

Yesu apacikidwa pamtanda

33 Ndipo pamene anafika ku malo dzina lace Bade, anampacika iye pamtanda pomwepo, ndi ocita zoipa omwe, mmodzi ku dzanja lamanja ndi wina kulamanzere.

34 Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa cimene acita. Ndipo anagawana zobvala zace, poyesa maere.

35 Ndipo anthu anaima alikupenya, Ndi akurunso anamlalatira iye nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Kristu wa Mulungu, wosankhidwa wace.

36 Ndipo asilikarinso anamnyoza, nadza kwa iye, nampatsa vinyo wosasa,

37 nanena, Ngati Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha.

38 Ndipo kunalinso lembo pamwamba pace, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YAAYUDA.

39 Ndipo mmodzi wa ocita zoipa anapacikidwawo anamcitira iye mwano nanena, Kodi suli Kristu Iwe? udzipulumutse wekha ndi ife.

40 Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku?

41 Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tirikulandira zoyenera zimene tinazicita: koma munthu uyu sanacita kanthu kolakwa.

42 Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukileni m'mene mulowa Ufumuwanu.

43 Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso.

44 Ndipo ora lace pamenepo linali ngati lacisanu ndi cimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lacisanu ndi cinai, ndipo dzuwa linada.

45 Ndipo nsaru yocinga ya m'Kacisi inang'ambika pakati.

46 Ndipo pamene Yesu anapfuula ndi mau akuru, anati, 1 Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wace.

47 Ndipo 2 pamene kenturiyo anaona cinacitikaco, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.

48 Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ici, pamene anaona zinacitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pacifuwa.

49 Ndipo 3 omdziwa iye onse, ndi akazi amene adamtsata kucokera ku Galileya, anaima kutari, naona zinthu izi.

Aika maliro a Yesu

50 Ndipo taonani, munthu dzina lace Yosefe, ndiye mkuru wa mirandu, munthu wabwino ndi wolungama

51 (amene sanabvomereza kuweruza kwao ndi nchito yao) wa ku Arimateya, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu,

52 yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wace wa Yesu.

53 Ndipo 4 anautsitsa, naukulunga m'nsaru yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaika munthu ndi kale lonse.

54 Ndipo panali tsiku lokonzera, ndi Sabata linayandikira.

55 Ndipo 5 akazi, amene anacokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wace.

56 Ndipo anapita kwao, 6 nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula 7 monga mwa lamulo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24