Luka 7 BL92

Kenturiyo wa ku Kapernao

1 Pamene Yesu adamariza mau ace onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao.

2 Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.

3 Ndipo pamene iye ana-I mva za Yesu, anatuma kwa iye akuru a Ayuda, namfunsa iye kuti adze kupulumutsa kapolo wace.

4 Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumcitire ici;

5 pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge.

6 Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika iye tsono pafupi panyumba yace, kenturiyo anatuma kwa iye abwenzi ace, kunena naye, Ambuye, musadzibvute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa;

7 cifukwa cace ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzaciritsidwa.

8 Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera akuru anga, ndiri nao asilikari akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tacita ici, nacita.

9 Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israyeli, cikhulupiriro cacikuru cotere.

10 Ndipo pakubwera ku nyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wacira ndithu.

Aukitsa mnyamata ku Nayini

11 Ndipo kunali, katapita kamphindi, iye ana pita kumudzi, dzina lace Nayini; ndipo ophunzira ace ndi mpingo waukuru wa anthu anapita nave.

12 Ndipo pamene anayandikira ku cipata ca mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amace ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye.

13 Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi cifundo cifukwa ca iye, nanena naye, Usalire.

14 Ndipo anayandikira, nakhudza cithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

15 Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amace.

16 Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace.

17 Ndipo mbiri yace imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira.

Amithenga a Yohane Mbatizi

18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi.

19 Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ace, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?

20 Ndipo pakufika kwa iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?

21 Nthawi yomweyo iye anaciritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zobvuta, ndi mizimu yoipa; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.

22 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

23 Ndipo wodala iye amene sakhomudwa cifukwa ca Ine.

24 Ndipo atacoka amithenga ace a Yohane, iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munaturuka kunka kucipululu kukapenya ciani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

25 Koma munaturuka kukaona ciani? Munthu wobvala zobvala zofewa kodi? Onani, iwo akubvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m'makuka a mafumu.

26 Koma munaturuka kukaona ciani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri.

27 Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye,Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere,Amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.

28 Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkuru woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

29 Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anabvomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

30 Koma Afarisi ndi acilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwa ndi iye.

31 Ndipo, ndidzafanizira ndi ciani anthu a mbadwo uno? ndipo afanana ndi ciani?

32 Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzace, ndi kunena, Ife tinakulizirani citoliro, ndipo inu simunabvina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai.

33 Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi ciwanda.

34 Mwana wa munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ocimwa!

35 Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ace onse.

Mkazi adzoza mapazi a Yesu

36 Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pacakudya.

37 Ndipo onani, mkazi wocimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pacakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino,

38 naimirira kumbuyo, pa mapazi ace, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ace ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wace, nampsompsonetsa mapazi ace, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.

39 Koma Mfarisi, amene adamuitana iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza iye, cifukwa ali wocimwa.

40 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anabvomera, Mphunzitsi, nenani.

41 Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ace a marupiya mazana asanu, koma mnzace makumi asanu.

42 Popeza analibe cobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Cotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

43 Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa,

44 Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene iye anaceukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lace.

45 Sunandipatsa mpsompsono wa cibwenzi; koma uyu sanaleka kupsompsonetsa mapazi anga, cilowere muno Ine.

46 Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma nyu anadzoza mapazi anga ndimafuta onunkhira bwmo.

47 Cifukwa cace, ndinena kwa iwe, Macimo ace, ndiwo ambiri, akhululukidwa; cifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.

48 Ndipo anati kwa mkazi, Macimo ako akhululukidwa.

49 Ndipo iwo akuseama naye pacakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso macimo?

50 Ndipo Iyeanati kwa mkaziyo, Cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24