Luka 5 BL92

Asodzi athandizidwa ndi Yesu, namtsata

1 Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;

2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m'mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adaturuka m'menemo, nalikutsuka makoka ao.

3 Ndipo iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yace ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.

4 Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.

5 Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.

6 Ndipo pamene anacita ici, anazinga unyinji waukuru wansomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika;

7 ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.

8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa.

9 Pakuti cizizwo cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;

10 ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

11 Ndipo m'mene iwo anakoceza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata iye.

Wakhate aciritsidwa

12 Ndipo panali, pamene iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipopameneanaona Yesu, anagwa nkhope yace pansi, nampempha iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.

13 Ndipo iye anatambalitsa dzanja lace, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka, Ndipo pomwepo khate linacoka kwa iye.

14 Ndipo iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu ali yense; koma ucoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa cikonzedwe cako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.

15 Koma makamaka mbiri yace ya iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhanakudzamvera, ndi kudzaciritsidwa nthenda zao.

16 Koma iye anazemba, nanka m'mapululu, nalikupemphera.

Yesu aciritsa munthu wamanjenfe

17 Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anacokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi iye yakuwaciritsa,

18 Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa iye.

19 Ndipo posapeza polowa naye, cifukwa ca unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wace, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

20 Ndipo iye, pakuona cikhulupiriro cao, anati, Munthu iwe, macimo ako akhululukidwa.

21 Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, ndani Uyu alankhula zomcitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira macimo, koma Mulungu yekha?

22 Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu?

23 Capafupi nciti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe macimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?

24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira macimo, (anati iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

25 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza cimene adagonapo, nacokapo, kunka kunyumba kwace, wakulemekeza Mulungu.

26 Ndipo cizizwo cinagwira anthu onse, ndipo analemekeza Mulungu nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.

Kuitanidwa kwa Levi

27 Ndipo zitatha izi iye anaturuka, Danna munthu wamsonkho, dzina lace Levi, alikukhala polandira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.

28 Ndipo iye anasiya zonse, nanyamuka, namtsata iye.

29 Ndipo Levi anamkonzera iye phwando lalikuru kunyumba kwace; ndipo panali khamu lalikuru la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pacakudya pamodzi nao.

30 Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ace nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ocimwa?

31 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo.

32 Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ocimwa kuti atembenuke mtima,

Za kudzikana kudya

33 Ndipo iwo anati kwa iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawiri kawiri, ndi kucita mapemphero; cimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.

34 Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?

35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.

36 Ndipo iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba cigamba ca maraya arsopano, naciphatika pa maraya akale; cifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi cigamba ca atsopanowo sicidzayenerana ndi akalewo.

37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; cifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.

38 Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano.

39 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24