Luka 22 BL92

Yudase apangana kupereka Yesu

1 Ndipo phwando la mikate yopanda cotupitsa linayandikira, ndilo lochedwa Paskha.

2 Ndipo ansembe akuru ndi alembi anafunafuna maphedwe ace pakuti anaopa anthuwoo.

3 Ndipo Satana analowa m'Yudase wonenedwa Isikariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo,

4 Ndipo iye anacoka, nalankhulana ndi ansembe akulu ndi akazembe mompereka iye kwa iwo.

5 Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama.

6 Ndipo iye anabvomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.

Paskha Iotsiriza. Mgonero

7 Ndipo tsiku la mikate yopanda cotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paskha.

8 Ndipo iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitanimutikonzere ife Paskha, kuti tidye.

9 Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti?

10 Ndipo iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.

11 Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Cipinda ca alendo ciri kuti, m'mene ndikadye Paskha pamodzi ndi ophunzira anga?

12 Ndipo iyeyo adzakuonetsani cipinda cacikuru capamwamba, cokonzeka; mukakonzere kumeneko.

13 Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paskha.

14 Ndipo itadza nthawi yace, iye anakhala pacakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi iye.

15 Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa;

16 pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.

17 Ndipo analandira cikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ici, mucigawane mwa inu nokha;

18 pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako cipatso ca mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.

19 Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, ici ndi thupi langa lopatsidwa cifukwa ca inu; citani ici cikumbukilo canga.

20 Ndipo coteronso cikho, atatha mgonero, nanena, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa cifukwa ca inu.

21 Koma onani, dzanja lace la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine.

22 Pakuti Mwana wa munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!

23 Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzacita ici.

Kutsutsana kwakuti wamkuru ndani

24 Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkuru.

25 Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awacitira ufumu; ndipo iwo amene awacitira ulamuliro anenedwa, Ocitira zabwino.

26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkuru mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

27 Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseama pacakudya kapena wakutumikirapo? si ndiye wakuseama pacakudya kodi? koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.

28 Koma inu ndinuamene munakhala ndi Ine cikhalire m'mayesero anga;

29 ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga;

30 ndipo mudzakhala pa mipando yacifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.

Yesu acenjeza Petro

31 Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;

32 koma ndinakupempherera kuti cikhulupiriro cako cingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.

33 Ndipo anati kwa iye, Ambuye, ndiripo ndikapite ndi Inu kundende ndikuimfa.

34 Ndipo iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine.

35 Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.

36 Ndipo anati kwaiwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse copfunda cace, nagule lupanga,

37 Pakuti ndinena ndi inu, cimene cidalembedwa ciyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine ziri naco cimariziro.

38 Ndipo iwo anati, Ambuye, taonani, malupanga awir siwa. Ndipo anati kwa iwo, Cakwa nira.

Yesu m'Getsemane

39 Ndipo iye anaturuka, napita monga adafucita, ku phiri la Azitona ndi ophunzira anamtsata iye.

40 Ndipo pofika pomwepo, anati kwa iwo, Pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.

41 Ndipo anapatukana nao kutalika kwace ngan kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,

42 nati, Atate, mukafuna Inu, cotsani cikho ici pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kucitike.

43 Ndipo anamuonekera iye 1 mngelo wa Kumwamba namlimbitsa iye.

44 Ndipo 2 pokhala iye m'cipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lace linakhala ngati madontho akuru a mwazi alinkugwa pansi.

45 Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi cisoni,

46 ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, 3 pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.

Amgwira Yesu

47 Pamene iye anali cilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wochedwa Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona iye.

48 Koma Yesu anati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi cimpsompsono kodi?

49 Ndipo m'mene iwo akumzinga iye anaona cimene citi cicitike, anati, Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi?

50 Ndipo wina wa iwo 4 anakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, namdula khutu lace lamanja.

51 Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lace, namciritsa.

52 Ndipo 5 Yesu anati kwa ansembe akulu ndi akapitao a Kacisi, ndi akuru, amene anadza kumgwira iye, Munaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wacifwamba?

53 Masiku onse, pamene ndinali ndi inu m'Kacisi, simunatansa manja anu kundigwira: koma 6 nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

Petro akana Yesu

54 Ndipo 7 pamenepo anamgwira iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutari.

55 Ndipo 8 pamene adasonkha mota m'kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao.

56 Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwace kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.

57 Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa iye.

58 Ndipo 9 popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine.

59 Ndipo 10 patapita ngati ora limodzi, wina ananenetsa, kuti, Zoonadi, munthu uyunso anali naye, pakuti ndiye Mgalileya.

60 Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa cimene ucinena, Ndipo pomwepo, iye ali cilankhulire, tambala analira.

61 Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo 11 Petra anakumbukila mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, 12 Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

62 Ndipo anaturuka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.

Yesu pa bwalo la akuru a Ayuda

63 Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza iye, nampanda.

64 Ndipo anamkulunga iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani?

65 Ndipo zambiri zina anamnenera iye, namcitira mwano.

66 Ndipo 13 pamene kunaca, bungwe la akuru a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe akuru ndi alembi; ndipo anapita naye ku bwalo lao, nanena, 14 Ngati uli Kristu, utiuze.

67 Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzabvomereza;

68 ndipo ndikakufunsani kanthu, simudzayankha.

69 Koma 15 kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala pa dzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.

70 Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo iye anati kwa iwo, 16 Munena kuti ndine.

71 Ndipo iwo anati, 17 Tifuniranjinso mboni? pakuti ife tokha tinamva m'kamwa mwa iye mwini.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24