Luka 24 BL92

Yesu auka kwa akufa

1 Koma tsiku loyamba la sabata, mbanda kuca, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza.

2 Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuucotsa pamanda.

3 Ndipo m'mene analowa sanapeza mtembo wa Ambuye Yesu.

4 Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru naco, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atabvala zonyezimira;

5 ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?

6 Palibe kuno iye, komatu anauka; kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya,

7 ndi kunena, kuti, Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ocimwa, ndi kupacikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lacitatu.

8 Ndipo anakumbukila mau ace, nabwera kucokera kumanda,

9 nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe.

10 Koma panali Mariya wa Magadala, ndi Y ohana, ndi Mariya amace wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.

11 Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zacabe, ndipo sanamvera akaziwo.

12 Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsaru zoyera pa zokha; ndipo anacoka nanka kwao, nazizwa ndi cija cidacitikaco.

Zocitika pa njira ya ku Emau

13 Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lace Emau, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi.

14 Ndipo iwowa anakambirana nkhani za izi zonse zidacitika.

15 Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.

16 Koma maso ao anagwidwa kuti asamzindikire iye.

17 Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zacisoni.

18 Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lace Kleopa, anayankha nati kwa iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m'Yerusalemu ndi wosazindikira zidacitikazi masiku omwe ano?

19 Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa iye, lzi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'nchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;

20 ndikuti ansembe akulu ndi akulu athu anampereka iye ku ciweruziro ca imfa, nampacika iye pamtanda.

21 Ndipo tinayembekeza ife kuti iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israyeli, Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lacitatu kuyambira zidacitika izi.

22 Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene analawirira kumanda;

23 ndipo m'mene sanapeza mtembo wace, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo iye.

24 Ndipo ena a iwo anali nafe anacoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuona.

25 Ndipo iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndiozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!

26 Kodi sanayenera Kristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wace?

27 Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za iye yekha.

28 Ndipo anayandikira ku mudzi umene analikupitako; ndipo anacita ngati anafuna kupitirira.

29 Ndipo anamuumiriza iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu, Ndipo analowa kukhala nao.

30 Ndipo kunali m'mene iye anaseama nao pacakudya, anatenga mkate, naudalitsa naunyema, napatsa iwo.

31 Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira iye; ndipo anawakanganukira iye, nawacokera.

32 Ndipo anati wina kwa mnzace, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitseguliramalembo?

33 Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi,

34 nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.

35 Ndipo iwo anawafotokozera za m'njira, ndi umo anadziwika nao m'kunyema kwa mkate.

Yesu aonekera kwa khumi ndi mmodziwo

36 Ndipo pakulankhula izi iwowa, iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu.

37 Koma anaopsedwandi kucita mantha, 1 nayesa alikuona mzimu.

38 Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji obvutika? ndipo matsutsano am auka bwanji m'mtima mwanu?

39 Penyani manja anga ndi mapazianga, kuti Ine ndine mwini: 2 ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe, mnofu ndi mafupa, monga muona ndirinazo Ine.

40 Ndipo m'mene ananena ici, anawaonetsera iwo manja ace ndi mapazi ace.

41 Koma pokhala iwo cikhalire osakhulupirira cifukwa ca cimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, 3 Muli nako kanthu kakudya kuno?

42 Ndipo anampatsa iye cidutsu ca nsomba yokazinga.

43 Ndipo 4 anacitenga, nacidya pamaso pao.

44 Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.

45 Ndipo 7 anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;

46 ndipo anati kwa iwo, 8 Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lacitatu;

47 ndi kuti kulalikidwe m'dzina lace kulapa ndi 9 kukhululukidwa kwa macimo kwa 10 mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.

48 11 Inu ndinu mboni za izi.

49 Ndipo onani, 12 Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwabvekedwa ndi mphamvu yocokera Kumwamba.

Yesu akwera kunka Kumwamba

50 Ndipo anaturuka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ace, nawadalitsa.

51 Ndipo kunali, 13 pakuwadalitsa iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba.

52 Ndipo 14 anamlambira iye, nabwera ku Yerusalemu ndi cimwemwe cacikuru;

53 ndipo IS anakhala ci khalire m'Kacisi, nalikuyamika Mulungu, Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24