Luka 2 BL92

Kubadwa kwa Yesu Kristu

1 Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linaturuka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;

2 ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya.

3 Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu ali yense ku mudzi wace.

4 Ndipo Yosefe yemwe anakwera kucokera ku Galileya, ku mudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, ku mudzi wa Davine, dzina lace Betelehemu, cifukwa iye anali wa banja ndi pfuko lace la Davine;

5 kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Mariya, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati,

6 Ndipo panali pokhaia iwo komweko, masiku ace a kubala anakwanira.

7 Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

Abusa a ku Betelehemu

8 Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.

9 Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru.

10 Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;

11 pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.

12 Ndipo ici ndi cizindikilo kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsaru atagonamodyera.

13 Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,

14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.

15 Ndipo panali, pamene angelo anacokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzace, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone cinthu ici cidacitika, cimene Ambuye anatidziwitsira ife.

16 Ndipo iwo anadza ndi cangu, napeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.

17 Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.

18 Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.

19 Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.

20 Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.

Kudulidwa ndi kuperekedwa kwa Yesu

21 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula iye, anamucha dzina lace Yesu, limene anachula mngeloyo asanalandiridwe iye m'mimba.

22 Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa cilamulo ca Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza iye kwa Ambuye,

23 (monga mwalembedwa m'cilamulo ca Ambuye, kuti mwamuna ali yense wotsegula pa mimba ya amace adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)

24 ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'citamulo ca Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.

Za Simeoni ndi za Anna

25 Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lace Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.

26 Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu wace wa Ambuye.

27 Ndipo iye analowa kuKacisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amace analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamcitira iye mwambo wa cilamulo,

28 pomwepo iye anamlandira iye m'manja mwace, nalemekeza Mulungu, nati,

29 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,Lolani ine, kapolo wanu, ndicoke mumtendere;

30 Cifukwa maso anga adaona cipulumutso canu,

31 Cimene munakonza pamaso pa anthu onse,

32 Kuunika kukhale cibvumbulutso ca kwa anthu a mitundu,Ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.

33 Ndipo atate ndi amace anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za iye.

34 Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Mariya amace, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa. Israyeli; ndipo akhale cizindikilo cakutsutsana naco;

35 eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.

36 Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa pfuko la Aseri; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wace, kuyambira pa unamwali wace,

37 zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zace: makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sanacoka kuKacisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.

38 Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za iye kwa anthu onse 1 akuyembekeza ciombolo ca Yerusalemu.

39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa cilamulo ca Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mudzi kwao, ku Nazarete.

40 Ndipo 2 mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu cinali pa iye.

Mnyamata Yesu pakati pa aphunzitsi

41 Ndipo atate wace ndi amace 3 akamuka caka ndi caka ku Yerusalemu ku Paskha.

42 Ndipo pamene iye anakhala ndi zaka zace khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga macitidwe a phwando;

43 ndipo pakumariza masiku ace, pakubwera iw, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amace sanadziwa;

44 koma iwo anayesa kuti iye ali m'cipiringu ca ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;

45 ndipo pamene sanampeza, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna iye.

46 Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza iye m'Kacisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.

47 Ndipo 4 onse amene anamva iye anadabwa ndi cidziwitso cace, ndi mayankho ace.

48 Ndipo m'mene anamuona iye, anadabwa; ndipo amace anati kwa iye, Mwanawe, wacitiranji ife cotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.

49 Ndipo iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine 5 ndikhale m'zace za Atate wanga?

50 Ndipo 6 sanadziwitsa mau amene iye analankhula nao.

51 Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo 7 amace anasunga zinthu izi zonse mumtima mwace.

52 Ndipo Yesu 8 anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'cisomo ca pa Mulungu ndi ca pa anthu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24