Luka 8 BL92

Akazi otumikira Yesu ndi cuma cao

1 Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza U thenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,

2 ndi akazi ena amene anaciritsidwa mizimu yoipa ndi nthenda zao, ndiwo, Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinaturuka mwa iye,

3 ndi Yohana, mkazi wace wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi eumacao.

Fanizo La Wofesa

4 Ndipo pamene khamu lalikuru la anthu linasonkhana, ndi anthu a ku midzi yonse anafika kwa iye, anati mwa fanizo:

5 Anaturuka wofesa kukafesa mbeu zace; ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya.

6 Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, cifukwa zinalibe mnyontho.

7 Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inapuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa.

8 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena iye izi anapfuula, iye amene ali ndi makutu akumva amve.

9 Ndipo ophunzira ace anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili liri lotani?

10 Ndipo iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse,

11 Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu,

12 Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nacotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

13 Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.

14 Ndipo zija zinagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi cuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

15 Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

Fanizo La nyali

16 Ndipo palibe munthu, atayatsa, nyali, aibvundikira ndi cotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pacoikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

17 Pakuti palibe cinthu cobisika, cimene sicidzakhala coonekera; kapena cinsinsi cimene sicidzadziwika ndi kubvumbuluka.

18 Cifukwa cace yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali naco; ndipo kwa iye amene alibe cidzacotsedwa, cingakhale cija aoneka ngati ali naco.

Amace ndi abale a Yesu

19 Ndipo anadza kwa iye amace ndi abale ace, ndipo sanakhoza ku: mfika, cifukwa ca khamu la anthu.

20 Ndipo anamuuza iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu.

21 Koma iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawacita.

Yesu atontholetsa namondwe

22 Ndipo panali limodzi la masiku aja, iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ace; nati kwa iwo, Tiolokere ku tsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.

23 Ndipo m'mene iwo anali kupita pamadzi, iye anagona tulo, Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

24 Ndipo anadza kwa iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika, Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ace a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa batao

25 Ndipo iye anati kwa iwo, Cikhulupiriro canu ciri kuti? Ndipo m'kucita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera iye?

Munthu wa ku Gerasa wogwidwa ndi mizimu yoipa

26 Ndipo iwo anakoceza kudooko ku dziko la Agerasa, ndilo Iopenyana ndi Galileya.

27 Ndipo ataturuka pamtanda iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanabvala cobvala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.

28 Ndipo pakuona Yesu, iye anapfuula, nagwa pansi pamaso pace, nati ndi mau akuru, Ndiri naco ciani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikupemphani Inu musandizunze.

29 Pakuti iye adalamula mzimu wonyansa uturuke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi ciwandaco kumapululu.

30 Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, cifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

31 Ndipo zinampempha iye, kuti asazilamulire zicoke kulowa kuphompho.

32 Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zirinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.

33 Ndipo ziwandazo zinaturuka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.

34 Ndipo akuwetawo m'mene anaona cimene cinacitika, anathawa, nauza a kumudzi ndi kumiraga yace.

35 Ndipo iwo anaturuka kukaona cimene cinacitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinaturuka mwa iye, alikukhala pansi ku mapazi ace a Yesu wobvala ndi wa nzeru zace; ndipo iwo anaopa.

36 Ndipo amene anaona anawauza iwo maciritsidwe ace a wogwidwa ciwandayo.

37 Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa Ioyandikira anamfunsa iye acoke kwa iwo; cifukwa anagwidwa ndi mantha akuru. Ndipo iye analowa m'ngalawa, nabwerera.

38 Ndipo munthuyo amene ziwanda zinaturuka mwa iye anampempha iye akhale ndi iye; koma anamuuza apite, nanena,

39 Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuruzo anakucitira iwe Mulungu. Ndipo iye anacoka, nalalikira ku mudzi wonse zazikuruzo Yesu anamcitira iye,

Mwana wamkaziwa Yairo. Mkazi wokhudza copfunda ca Yesu

40 Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira iye; pakuti onse analikumlindira iye.

41 Ndipo onani, panadza munthu dzina lace Yairo, ndipo iye ndiye mkuru wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ace a Yesu, nampempha iye adze kunyumba kwace;

42 cifukwa anali naye mwana wamkazi mmodzi yekha, wa zaka zace ngati khumi ndi ziwiri, ndipo analinkumwalira iye, Koma pakupita iye anthu a mipingo anakanikizana naye,

43 Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wace zonse, ndipo sanathe kuciritsidwa ndi mmodzi yense,

44 anadza pambuyo pace, nakhudza mphonje yacobvala cace; ndipo pomwepo nthenda yace inaleka.

45 Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.

46 Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti a ndazindikira Ine kuti mphamvu yaturuka mwa Ine.

47 Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pace, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cace ca kumkhudza iye, ndi kuti anaciritsidwa pomwepo.

48 Ndipo iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

49 M'mene iye anali cilankhulire, anadza wina wocokera kwa mkuru wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usambvute Mphunzitsi.

50 Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.

51 Ndipo pakufika iye kunyumbako, sanaloleza wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amace.

52 Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudzigugudapacifuwa. Koma iye anati, Musalire; pakuti iye sanafa, koma agona tulo.

53 Ndipo anamseka iye pwepwete podziwa kuti anafa.

54 Ndipo iye anamgwira dzanja lace, naitana, nati, Buthu, tauka.

55 Ndipo mzimu wace unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya.

56 Ndipo atate wace ndi amace anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu ali yense cimene cinacitika.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24