Luka 6 BL92

Yesu Mbuye wa tsiku la Sabata

1 Ndipo kunali tsiku la Sabata, iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ace analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya.

2 Koma Afarisi ena anati, Mucitiranji cosaloledwa kucitika tsiku la Sabata?

3 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale cimene anacita Davine, pamene paja anamva Njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi,

4 kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?

5 Ndipo iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata.

Aciritsa munthu wa dzanja lopuwala

6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, iye analowa m'sunagoge naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lace lamanja linali lopuwala.

7 Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda iye, ngati adzaciritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze comneneza iye.

8 Koma iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lace lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.

9 Ndipo Iyeananyamuka, naimirira. Ndipo Yesuanati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kucita zabwino, kapena kucita zoipa? kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?

10 Ndipo pamene anaunguza-unguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako, Ndipo iye anatero, ndi dzanja lace lina; bwerera momwe.

11 Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzace kuti amcitire Yesu ciani.

Yesu asankha ophunzira khumi ndi awiri

12 Ndipo kunali masiku awa, iye anaturuka nanka kuphiri kukapemphera; nacezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.

13 Ndipo kutaca, anaitana ophunzira ace; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawachanso dzina lao atumwi:

14 Simoni, amene anamuchanso Petro, ndi Andreya mbale wace, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo,

15 ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wochedwa Zelote,

16 ndi Yuda mwana wa Yakobo, ndi Yudase Isikariote, amene anali wompereka iye.

Ciphunzitso ca paphiri

17 Ndipo iye anatsika nao, naima pacidikha, ndi khamu lalikuru la ophunzira ace, nw unyinji waukuru wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene anadza kudzamva iye ndi kudzaciritsidwa nthenda zao;

18 ndipo obvutidwa ndi mizimu yonyansa anaciritsidwa,

19 ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza iye; cifukwa munaturuka mphamvu mwa iye, niciritsa onsewa.

20 Ndipo iye anakweza maso ace kwa ophunzira ace, nanena, Odala osauka inu; cifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

21 Odala inu akumva njala tsopano; cifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; cifukwa mudzaseka.

22 Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, cifukwa ca Mwana wa munthu.

23 Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi cimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikuru Kumwamba; pakuti makolo ao anawacitira aneneri zonga zomwezo.

24 Koma tsoka inu eni cuma! cifukwa mwalandira cisangalatso canu.

25 Tsoka inu okhuta tsopano! cifukwa mudzamva njala, Tsoka inu, akuseka tsopano! cifukwa mudzacita maliro ndi kulira misozi.

26 Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! pakuti makolo ao anawatero momwemo ananeri onama.

27 Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; citirani zabwino iwo akuda inu,

28 dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akucitira inu cipongwe.

29 Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzace; ndi iye amene alanda copfunda cako, usamkanize malaya ako.

30 Munthu ali yense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.

31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.

32 Ndipo 1 ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti ocimwa omwe akonda iwo akukondana nao.

33 Ndipo ngati muwacitira zabwino iwo amene akucitirani, inu zabwino, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti anthu ocimwa omwe amacita comweco.

34 Ndipo 2 ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti inde anthu ocimwa amakongoletsa kwa ocimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.

35 Koma 3 takondanani nao adani anu, ndi kuwacitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikuru, ndipo 4 inu mudzakhala ana a Wamkurukuruyo; cifukwa iye acitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

36 Khalani inu acifundo monga Atate wanu ali wacifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

37 Ndipo 5 musawatsutsa, ndipo simudzatsutsidwa. Masulani, ndipo mudzamasulidwa.

38 6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

39 Ndipo iye ananenanso nao fanizo, 8 Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzace wakhungu? kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna?

40 9 Wophunzira saposa mphunzitsi wace; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wace.

41 Ndipo uyang'aniranji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira?

42 10 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndicotse kacitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! thanga wacotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kucotsa kacitsotso ka m'diso la mbale wako.

43 Pakuti 11 palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zobvunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino,

44 Pakuti 12 mtengo uli wonse uzindikirika ndi cipatso cace. Pakuti anthu samachera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samachera mphesa,

45 13 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cokoma ca mtima wace; ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'coipa cace: pakuti m'kamwa mwace mungolankhula mwa kucuruka kwa mtima wace.

46 Ndipo 14 mundichuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusacita zimene ndizinena?

47 15 Munthu ali yense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwacita, ndidzakusonyezani amene afanana naye.

48 Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza cigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; cifukwa idamangika bwino.

49 Koma iye amene akumva, ndi kusacita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwace kwa nyumbayo kunali kwakukuru.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24