Luka 13 BL92

Maphedwe a Agalileya, tsanfa la Siloamu

1 Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao.

2 Ndipo iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akucimwa koposa Agalileya onse, cifukwa anamva zowawa izi?

3 Ndinena kwa inu, iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.

4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?

5 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse ci, modzimodzi.

Fanizo la mkuyu wosabala

6 Ndipo iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wookam'munda wace wamphesa. Ndipo anadza nafuna cipatso pa uwu, koma anapeza palibe.

7 Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna cipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pace?

8 Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale caka cino comwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;

9 ndipo, ngati udzabala cipatso kuyambira pamenepo, cabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

Aciritsa mkazi wopeteka

10 Ndipo analikuphunzitsa m'sungagoge mwina, tsiku la Sabata.

11 Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.

12 Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.

13 Ndipo anaika manja ace pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.

14 Ndipo mkuru wa sunagoge anabvutika mtima, cifukwa Yesu anaciritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira nchito, cifukwa cace idzani kudzaciritsldwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.

15 Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu ali yense wa inu samaimasula ng'ombe yace, kapena buru wace kucodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?

16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yace imeneyi tsiku la Sabata?

17 Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinacitidwa ndi iye.

Fanizo la mpiru ndi la cotupitsa

18 Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi ciani? ndipo ndidzaufanizira ndi ciani?

19 Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wace wace, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zace.

20 Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi ciani?

21 Ufanana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazianatenga, nacibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupa wonsewo,

Khomo lopapatiza

22 Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.

23 Ndipo munthu anati kwa iye, Ambuye, akupulumutsidwandiwo owerengeka kodi? Koma iye anati kwa iwo,

24 Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; cifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.

25 Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pacitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene mucokerako;

26 pomwepo mudzayambakunena, Ifetinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m'makwalala a kwathu;

27 ndipo iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene mucokera inu; cokani pa Ine, nonse akucita cosalungama,

28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu. Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha muturutsidwa kunja.

29 Ndipo anthu adzacokera kum'mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwela, nadzakhalapansi mu Ufumu wa Mulungu.

30 Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.

Amcenjeza Yesu za Herode. Yesu alirira Yerusalemu

31 Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa iye, Turukani, cokani kuno; cifukwa Herode afuna kupha lou.

32 Ndipo iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditurutsa ziwanda, nditsiriza maciritso lero ndi mawa, ndipo mkuca nditsirizidwa.

33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkuca, cifukwa sikuloleka kuti mneneri aonongeke kunja kwace kwa Yerusalemu.

34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! ha! kawiri kawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ace m'mapiko ace, ndipo simunafunai!

35 onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka iye amene akudza m'dzina la Ambuye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24